У нас вы можете посмотреть бесплатно CDEDI PRESS BRIEFING - NAMIWA WATOKOTA ZA MAVUTO A FUEL| ATOLANKHANI AMPANIKIZA NDI MAFUNSO AWA или скачать в максимальном доступном качестве, видео которое было загружено на ютуб. Для загрузки выберите вариант из формы ниже:
Если кнопки скачивания не
загрузились
НАЖМИТЕ ЗДЕСЬ или обновите страницу
Если возникают проблемы со скачиванием видео, пожалуйста напишите в поддержку по адресу внизу
страницы.
Спасибо за использование сервиса ClipSaver.ru
Bungwe la Center for Democracy and Economic Development Initiatives (CDEDI) lapempha boma kuti lichite mgwilizano ndi maiko komanso makampani omwe amagulitsa mafuta agalimoto zomwe zithandizile dziko lino kukhala ndi mafuta agalimoto otsika mtengo. Mkulu wabungweli a Sylvester Namiwa ayankhula izi pa msonkhano wa atolankhani omwe bungweli likuchititsa ku munzinda wa Lilongwe. Malingana ndi a Namiwa, dziko lino likukumana ndimavuto okhudza mafuta agalimoto kaamba koti chipani chakale cholamula cha Malawi Congress (MCP) chinasokoneza ndondomeko zoyenela zakagulidwe kamafuta. Apa Iwo ati bungwe lawo lichita kafukufuku ndikubweletsa poyela zifukwa zomwe boma lakwezela mitengo ya mafuta agalimoto ndikupitilita kupempha boma kutsitsa mtengo wamafutawa. Pakadalipano, a Namiwa ati akuyembekezela kuti boma lichitapo kanthu potsitsa mtengo wa mafutawa potengela kuti mtsogoleri wadziko lino Professor Arthur Peter Mutharika amamva madandaulo a anthu.